Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 18:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Nduna za Saulo zidamuuza Davide mau amenewo. Koma iye adati, “Kani mukuchiyesa chinthu chapafupi kukhala mkamwini wa mfumu? Kodi simukuwona kuti ndine wosauka ndi wosatchuka?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 18:23
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.


Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.


Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu.


Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka.


Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde.


Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani mu Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?


Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.


Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide.


Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa