Ndipo Abinere analankhula nao akulu a Israele nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;
1 Samueli 8:4 - Buku Lopatulika Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono akuluakulu onse a Aisraele adasonkhana nadza kwa Samuele ku Rama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. |
Ndipo Abinere analankhula nao akulu a Israele nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;
Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.
Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;
Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye.
Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu.
Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.