Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
1 Samueli 5:10 - Buku Lopatulika Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adatumiza Bokosi lachipanganolo ku Ekeroni. Koma litangofika ku Ekeroniko, anthu akumeneko adalira kuti, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele, abwera nalo kwathu kuno, kuti atiphetse ife pamodzi ndi anthu athu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni. Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.” |
Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.
ndi Zabadi mwana wake, ndi Sutela mwana wake, ndi Ezere, ndi Eleadi, amene anthu a Gati obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.
ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.
Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?
kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;
natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.
Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake.
Ndipo anthu a Israele ndi Ayuda ananyamuka, nafuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka kufika kuchigwako, ndi ku zipata za Ekeroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa panjira ya ku Saaraimu, kufikira ku Gati ndi ku Ekeroni.
Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mzinda monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo.
Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.