2 Mafumu 1:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Tsiku lina mfumu Ahaziya ali ku likulu lake ku Samariya, adagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake cham'mwamba, navulala kwambiri. Ndiye adatuma amithenga naŵauza kuti, “Pitani, mukafunse kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, ngati nditi ndichire.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake chammwamba ku Samariya, ndipo anavulala kwambiri. Choncho iye anatuma amithenga nawawuza kuti, “Pitani mukafunse kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, ngati ndichire matendawa.” Onani mutuwo |
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.