Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:3 - Buku Lopatulika

3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma mngelo wa Chauta adauza mneneri Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ukaŵafunse kuti, ‘Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukupita kukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:3
21 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.


Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.


Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye.


Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakukanika.


Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati,


Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.


Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.


Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m'chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.


Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.


Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israele.


Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele.


Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?


Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.


Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.


Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa