Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:4 - Buku Lopatulika

4 Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Nchifukwa chake tsono mau a Chauta oti mukauze mfumu ndi aŵa: ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Ndipo Eliya adapita.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:4
14 Mawu Ofanana  

koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.


Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai;


Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mzinda mwanayo adzatsirizika.


Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.


Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.


Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera chifukwa ninji?


Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.


Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.


Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.


Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.


Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa