Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 6:2 - Buku Lopatulika

2 Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pitani ku mzinda wa Kaline mukaone. Mupitenso ku Hamati mzinda wotchuka uja, tsono mutsikire ku Gati kwa Afilisti. Kodi Aisraelenu mukupambana anthu a mafumu ameneŵa? Kodi kapena dziko lao nlalikulu kupambana lanu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane; mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja, ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti. Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa? Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 6:2
19 Mawu Ofanana  

Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.


Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere,


Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.


Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m'mizinda ya Samariya, m'malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m'mizinda mwake.


Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima,


Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?


Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?


popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga mizinda m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti.


Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete.


Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pamtsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja?


Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.


Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi.


Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu.


Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa