Amosi 6:1 - Buku Lopatulika1 Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira! Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira! Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsoka kwa inu amene mumakhala mosatekeseka ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya. Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Aisraele, inu amene anthu onse amafika kwanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya, inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka, kumene Aisraeli amafikako! Onani mutuwo |
Pamenepo amuna asanuwa anachoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhala okhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakuchititsa manyazi m'chinthu chilichonse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu aliyense.