Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:27 - Buku Lopatulika

27 M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira mzinda wa Damasiko.” Akutero Chauta, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:27
10 Mawu Ofanana  

Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova.


Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.


Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzindawu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira.


Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!


Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.


Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa