1 Samueli 26:18 - Buku Lopatulika Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chifukwa chiyani mbuyanga mukundilondola ine mtumiki wanu? Kodi ndachita chiyani? Kodi tchimo langa nlotani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukundilonda ine mtumiki wanu? Kodi ine ndachita chiyani ndipo ndapezeka ndi cholakwa chotani? |
Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa, anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa.
Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.
Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?
Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala?
Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula choipa, chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji?
Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?
Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa.