1 Samueli 20:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Davide anathawa ku Nayoti mu Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsono Davide adathaŵa ku Nayoti ku Rama, nabwera kwa Yonatani. Ndipo adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndidachita chiyani? Ndidalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndidaŵachimwira chiyani, kuti azifuna kundipha?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.