Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.
1 Samueli 22:6 - Buku Lopatulika Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala mu Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala m'Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Saulo adamva kuti Davide ndi anthu ake adapezeka. Tsiku limenelo Sauloyo adaakhala pansi patsinde pa mtengo wa mbwemba womera pa chitunda china ku Gibea, mkondo uli m'manja, ankhondo ake atamzungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sauli anamva kuti Davide ndi anthu ake apezeka. Nthawiyo nʼkuti Sauli atakhala pansi pa mtengo wa bwemba pa phiri la ku Gibeya, mkondo uli mʼdzanja lake ndi ankhondo ake atayima chomuzungulira. |
Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse.
Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze.
Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;
Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo.
Ndipo mzimu woipa wochokera kwa Yehova unali pa Saulo, pakukhala iye m'nyumba mwake, ndi mkondo wake m'dzanja lake; ndipo Davide anaimba ndi dzanja lake.
Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.
Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli mu Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.