1 Samueli 21:4 - Buku Lopatulika Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wansembeyo adayankha kuti, “Pano ndilibe buledi wamba, koma alipo ndi buledi wachipembedzo. Ngati anthu anu sadakhale ndi akazi ao, angathe kudya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma wansembeyo anamuyankha Davide kuti, “Ine ndilibe buledi wamba woti ndikupatseni. Koma pali buledi wachipembedzo yekha. Ngati anthu amene muli nawo sanagone ndi akazi awo mukhoza kudya.” |
Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho.
Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.