Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
1 Samueli 2:6 - Buku Lopatulika Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta amadzetsa imfa ndipo amabwezeranso moyo, amatsitsira ku manda, ndipo amaŵatulutsakonso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo, amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso. |
Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.
Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.
Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.
Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israele.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.
pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.
Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.
ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.