Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:20 - Buku Lopatulika

20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Ngakhale mwandionetsa mavuto ambiri owawa, mudzabwezeretsanso moyo wanga; kuchokera kunsi kwa dziko lapansi, mudzandiukitsanso.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:20
26 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene.


Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu.


Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.


Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu.


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.


Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake.


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.


Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?


yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.


Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa