Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 71:19 - Buku Lopatulika

19 Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zazikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zachikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu, zimafikira mpaka kumwambamwamba. Pali yani wofanafana nanu, Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba. Ndani wofanana nanu Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 71:19
20 Mawu Ofanana  

amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Kudziwa ichi kundiposa ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.


Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.


Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo.


Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.


Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.


Nzeru italikira chitsiru; satsegula pakamwa kubwalo.


Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?


Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.


koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo.


Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake lili loyera.


Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena padziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa