2 Mafumu 5:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Koma mfumu ya ku Israele ija itaŵerenga kalatayo, idang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni, ndipo idati, “Kodi ine ndine Mulungu amene amapha ndi kupatsanso moyo, kuti munthu ameneyu azindilembera mau oti ndichize khate la munthu wake? Nchodziŵikiratu kuti iyeyo akungofuna chifukwa choti ayambane nane.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!” Onani mutuwo |