Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.
1 Samueli 2:27 - Buku Lopatulika Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali mu Ejipito, m'nyumba ya Farao? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Ejipito, m'nyumba ya Farao? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina munthu wa Mulungu adafika kwa Eli namuuza kuti, “Chauta akuti, ‘Suja ndidadziwulula kwa banja la kholo lako Aroni pamene anali akapolo a Farao ku Ejipito? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto? |
Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.
Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.
Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;
Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye paphiri la Mulungu, nampsompsona.
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.
pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;
Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera mu Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo;
Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.
Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.
Koma ananena naye, Onatu, m'mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.