1 Samueli 9:6 - Buku Lopatulika6 Koma ananena naye, Onatu, m'mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Koma mnyamatayo adati, “Mumzindamu muli munthu wa Mulungu, munthu amene onse amamchitira ulemu. Zonse zimene amanena zimachitikadi. Bwanji tipite kumeneko. Mwina mwake angathe kutiwuza za ulendo wathuwu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.” Onani mutuwo |