Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 13:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono mneneri wa Mulungu adachokera ku Yuda napita ku Betele monga momwe Chauta adaamlamulira. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 13:1
23 Mawu Ofanana  

Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,


Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.


Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.


Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la paguwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova.


Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.


Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.


Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.


Anatinso, Chizindikiro ichi ndichiona nchiyani? Namuuza anthu a m'mzindawo, Ndicho manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazichitira guwa la nsembe la ku Betele.


Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa mu Kachisi wa Yehova kufukiza paguwa la nsembe la chofukiza.


natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.


Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?


Ndipo mizinda ya Yuda ndi okhala mu Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.


Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvere.


ndipo Ababiloni, olimbana ndi mzinda uwu, adzafika nadzayatsa mzindawu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.


koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.


Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.


Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.


Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali mu Ejipito, m'nyumba ya Farao?


Koma ananena naye, Onatu, m'mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa