Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo.
1 Samueli 2:26 - Buku Lopatulika Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monsemo mnyamata uja Samuele ankakulabe mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Chauta ndi anthu omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mnyamata Samueli anapitirira kukula mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Yehova ndi anthu. |
Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo.
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.
Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.
Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.