Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana aamuna atatu, ndi ana aakazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Chauta adadalitsadi Hana, ndipo adabala ana aamuna atatu ndi ana aakazi aŵiri. Ndipo mnyamata uja Samuele ankakula akutumikira Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo Yehova anamukomera mtima Hana. Anakhala ndi pathupi ndi kubereka ana aamuna atatu ndi ana aakazi awiri. Ndipo Samueli ankakula pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:21
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena.


Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.


motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.


Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.


Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.


Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa.


Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima.


Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa