Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
1 Samueli 18:3 - Buku Lopatulika Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adachita naye chipangano chifukwa ankamkonda monga momwe ankadzikondera iye mwini. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. |
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.
kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe?
Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake.