Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyake Mwejipito.
1 Samueli 16:18 - Buku Lopatulika Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mmodzi mwa antchitowo adati, “Ndaona mwana wamwamuna wa Yese wa ku Betelehemu amene ali wokhoza zeze, munthu wolimba mtima, ngwazi pankhondo, wochenjera polankhula, munthu wokongola. Ndipo Chauta ali naye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmodzi mwa antchito ake anati, “Ine ndinaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu. Ndiye munthu wodziwa bwino kuyimba, wolimba mtima, ngwazi pa nkhondo, wodziwa kuyankhula ndi wokongola. Ndipotu Yehova ali ndi iye.” |
Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyake Mwejipito.
Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.
Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi.
Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu.
Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.
Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine.
Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.
Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.