Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 16:19 - Buku Lopatulika

19 Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Choncho Saulo adatuma amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Tumizire Davide mwana wako, uja amaŵeta nkhosayu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndipo Sauli anatumiza amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Nditumizireni mwana wanu Davide, amene amaweta nkhosa.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 16:19
12 Mawu Ofanana  

Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.


Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake.


Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.


Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.


Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.


Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.


Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa