Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;
1 Samueli 11:1 - Buku Lopatulika Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita ngati mwezi umodzi, Nahasi Mwamoni adanka ndi gulu lankhondo kukazinga mzinda wa Yabesi m'dziko la Giliyadi. Tsono anthu onse a mu mzinda wa Yabesi adapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe chipangano, ndipo tidzakutumikirani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.” |
Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe;
Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.
Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,
Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.
Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza mizinda ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda mu Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera mu Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.
anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.
Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake;
Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;
nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.
ndipo inatenga wa mbumba yachifumu, nkuchita naye pangano, nkumlumbiritsa, nkuchotsa amphamvu a m'dziko;
Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;
Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.
Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano.
Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.
Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga.