Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 17:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi Mwamoni wochokera ku Raba, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndiponso Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wochokera ku Raba ku dziko la Amoni ndi Makiri mwana wa Amieli wochokera ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 17:27
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mzinda wachifumu.


Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi.


Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara.


Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.


Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.


Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa