Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 40:14 - Buku Lopatulika

14 nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Adamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaele, mwana wa Netaniya kuti adzakupheni?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sadaŵakhulupirire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 40:14
15 Mawu Ofanana  

Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.


Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni,


Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa,


pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao.


Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi mu Mizipa.


Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala mu Mizipa, ana aakazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala mu Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.


Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa