Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono pamene mudaona kuti Nahasi, mfumu ya Aamoni, adadza kuti adzamenyane nane, mudandiwuza kuti, ‘Iyai, koma mfumu ndiyo imene idzatilamulire,’ chonsecho mfumu yanu inali Chauta, Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.


Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Chomwecho pamene Ayuda onse okhala mu Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi mu Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao;


Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'mizinda yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?


Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.


Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.


koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;


koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.


Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa