Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Choncho Chauta adatuma Yerubaala, Balaki, Yefita ndi ine Samuele. Tidakupulumutsani kwa adani anu amene ankakuzingani, ndipo mudakhala pa mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:11
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale.


Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Giliyadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.


Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?


Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israele m'dzanja la Midiyani. Sindinakutume ndi Ine kodi?


Koma Yowasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? Iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lake la nsembe.


Chifukwa chake anamutcha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenere mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lake la nsembe.


Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, paphiri la More m'chigwa.


Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m'nyumba ya iye yekha.


osachitira chifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anachitira Israele.


Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova.


Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa