Chikhalidwe cha munthu woona wa MulunguSalimo la Davide. 1 Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? 2 Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. 3 Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake. 4 M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai. 5 Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi