Yehova asunga anthu ake nalanga oipaKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame? 2 Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima. 3 Akapasuka maziko, wolungama angachitenji? 4 Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake. 5 Yehova ayesa wolungama mtima, koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa. 6 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao. 7 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi