Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 11:6 - Buku Lopatulika

6 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iye adzaŵagwetsera makala ndi miyala yamoto ngati mvula, adzaŵalanga ndi mphepo yotentha monga kuŵayenera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 11:6
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;


Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.


Msampha woponda umbisikira pansi, ndi msampha wa chipeto panjira.


Adzakhala m'hema mwake iwo amene sali ake; miyala ya sulufure idzawazika pokhala pake.


Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye.


Anawapatsa mvula yamatalala, lawi la moto m'dziko lao.


Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.


Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto.


Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.


Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosakanizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a padziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.


Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza.


atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ake, Taona, ndachotsa m'dzanja mwako chikho chonjenjemeretsa, ngakhale mbale ya chikho cha ukali wanga; iwe sudzamwa icho kawirinso.


Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho mu ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala aakulu adzalitha mu ukali wanga.


Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulufure.


Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako.


koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu udavumba moto ndi sulufure zochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo;


Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi?


Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao;


Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa