Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Yohane 9:2 - Buku Lopatulika Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?” |
Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi?
Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.
Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.