Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 9:3 - Buku Lopatulika

3 Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 9:3
16 Mawu Ofanana  

Taonani, ndidziwa maganizo anu, ndi chiwembu mundilingirira moipa.


Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.


Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.


Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?


Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.


Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa