Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Yohane 7:11 - Buku Lopatulika Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulu a Ayuda ankamufunafuna kuchikondwereroko, nkumafunsana kuti, “Kodi amene uja ali kuti?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?” |
Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?
Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzake poimirira iwo mu Kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuchikondwerero kodi?
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.