Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 7:15 - Buku Lopatulika

15 Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Akulu a Ayuda adadabwa nati, “Bwanji munthu ameneyu ali ndi nzeru zotere, pamene sadaphunzire konse?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:15
18 Mawu Ofanana  

ndipo buku laperekedwa kwa wosadziwa kuwerenga, ndi kuti, Werengani umu; koma ati, Ine sindinaphunzire.


Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi?


Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo.


Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi chiphunzitso chake.


Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.


Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja?


Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda.


Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero.


Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa