Yohane 6:4 - Buku Lopatulika Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chikondwerero chija chachipembedzo chotchedwa Paska chidaayandikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi. |
Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.