Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 12:1 - Buku Lopatulika

1 Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Atatsala masiku asanu ndi limodzi kuti chifike chikondwerero cha Paska, Yesu adadza ku Betaniya, kumene kunali Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 12:1
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko.


Ndipo Iye analowa mu Yerusalemu, mu Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.


Ndipo anatuluka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa.


Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,


Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.


Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka.


Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.


Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.


M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,


Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero.


Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa