Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Yohane 3:9 - Buku Lopatulika Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nikodemo adafunsa kuti, “Zimenezi zingachitike bwanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?” |
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.
Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa?
Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu.
Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?
Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?