Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 21:3 - Buku Lopatulika

Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo mu usiku muja sanagwire kanthu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Simoni Petro adaŵauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakaloŵa m'chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.

Onani mutuwo



Yohane 21:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.


Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwe kuti ndiye Yesu.


ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema.


Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.


Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.


Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?


Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.