Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata yako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.
Yohane 2:6 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo. |
Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata yako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,