Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 16:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata yako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iye adati, ‘Mafuta amuyeso wokwanira mitsuko makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, khala pansi msanga, ungolembapo mitsuko makumi asanu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’ “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 16:6
7 Mawu Ofanana  

Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba.


Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?


Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wake, nanena kwa woyamba, Unakongola chiyani kwa mbuye wanga?


Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata yako nulembere makumi asanu ndi atatu.


Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.


Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.


osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa