ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
Yohane 2:3 - Buku Lopatulika Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “Waŵathera vinyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.” |
ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.
Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.
pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.