Yohane 2:1 - Buku Lopatulika Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati mu Kana wa mu Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, |
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.
Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.
Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.