Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:46 - Buku Lopatulika

46 Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala m'Kapernao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Yesu adapitanso ku mudzi wa Kana ku Galileya, kumene Iye adaasandutsa madzi vinyo kuja. Panali Nduna ina ya mfumu imene mwana wake ankadwala ku Kapernao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:46
14 Mawu Ofanana  

Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.


Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu.


Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.


ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:


M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.


chifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu a mipingo anakanikizana naye.


Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka.


Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.


ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa