Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 4:45 - Buku Lopatulika

45 Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita m'Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Komabe pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira popeza kuti eniakewo nawonso adaapita ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Paska, ndipo adaaona zonse zimene Yesu adaachita pachikondwereropo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 4:45
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasakaniza mwazi wao ndi nsembe zao.


Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.


Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu.


Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.


Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.


Ichi ndi chizindikiro chachiwiri Yesu anachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa mu Galileya.


Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa