Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Yohane 10:9 - Buku Lopatulika Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. |
Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.
Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.
Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.