Yohane 1:3 - Buku Lopatulika Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa. |
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;
Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.
Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye.
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.
ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;
Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwe kuchokera mu zoonekazo.
Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.
Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.