chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.
Numeri 9:23 - Buku Lopatulika Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. |
chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Monga ng'ombe zotsikira kuchigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; chomwecho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.
Ndipo simunasunge udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira nokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika.
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.
simunasiye abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu.